Luka 9 BL92

Yesu atuma ophunzira ace kukalalikira mau

1 Ndipo iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuciritsa nthenda.

2 Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuciritsa anthu odwala.

3 Ndipo iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndarama; ndipo musakhale nao malaya awiri.

4 Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikacokera kumeneko.

5 Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene muturuka m'mudzi womwewo, sansani pfumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

6 Ndipo iwo anaturuka, napita m'midzi m'midzi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuciritsa ponse.

Herode ndi Yohane Mbatizi

7 Ndipo Herode ciwangaco anamva mbiri yace ya zonse zinacitika; ndipo inamthetsa nzeru, cifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa;

8 koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka.

9 Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona iye.

Yesu acurukitsa mikate

10 Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera iye zonse anazicita. Ndipo iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka ku mudzi dzina lace Betsaida.

11 Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, naciritsa amene anasowa kuciritsidwa.

12 Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite ku midzi yoyandikira ndi kumiraga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; cifukwa tiri ku malo acipululu kuno.

13 Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tiribe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

14 Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma iye anati kwa ophunzira ace, Khalitsani iwo pansi magulu magulu, ngati makumi asanu asanu.

15 Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

16 Ndipo iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.

17 Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri.

Petro abvomereza Kristu

18 Ndipo kunali, pamene iye analikupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?

19 Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.

20 Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Kristu wa Mulungu.

21 Ndipo iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ici kwa munthu ali yense;

22 nati, Kuyenera kuti Mwana wa munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akuru, ndi ansembe akuru, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lacitatu.

Za kusenza mtanda

23 Ndipo iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wace tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

24 Pakutiamene ali yense akafuna kupulumutsa moyo wace, iye adzautaya; koma amene ali yense akataya moyo wace cifukwa ca Ine, iye adzaupulumutsa uwu.

25 Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wace?

26 Pakuti amene ali yense: adzacita manyazi cifukwa ca Ine ndi mau anga, Mwana wa munthu adzacita manyazi cifukwa ca iye, pamene adzafika ndi ulemerero wace ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.

27 Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

Mawalitsidwe a Yesu paphiri

28 Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.

29 Ndipo m'kupemphera kwace, maonekedwe a nkhope yace anasandulika, ndi cobvala cace cinayera ndi kunyezimira.

30 Ndipo onani, analikulankhulana nayeamuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;

31 amene anaonekera m'ulemerero, nanenaza kumuka kwace kumene iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu.

32 Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wace, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi iye.

33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tiri pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye cimene alikunena.

34 Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo.

35 Ndipo munaturuka mau mumtambo nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani iye.

36 Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala cete, ndipo sanauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.

Aciritsa mwana wodwala khunyu

37 Ndipo panali, m'mawa mwace, atatsika m'phiri, khamu lalikuru la anthu linakomana naye.

38 Ndipo onani, anapfuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; cifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:

39 ndipo onani, umamgwira iye mzimu, napfuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumcititsa thobvu pakamwa, nucoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye.

40 Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti auturutse; koma sanathe.

41 Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? idza naye kuno mwana wako.

42 Ndipo akadadza iye, ciwandaco cinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa, Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, naciritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wace.

43 Ndipo onse anadabwa pa ukulu wace wa Mulungu.Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazicita, iye anati kwa ophunzira ace,

44 Alowe mau ame: newa m'makutu anu; pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu.

45 Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.

Wamkulu m'Ufumu wa Kumwamba

46 Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani.

47 Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,

48 Amene ali yense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkuru.

Osatsutsana nafe athandizana nafe

49 Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.

50 Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

Asamariya amkaniza Yesu

51 Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe iye kumwamba, Yesu anatsimika kuloza nkhope yace kunka ku Yerusalemu,

52 natumiza amithenga patsogolo pace; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera iye malo.

53 Ndipo iwo sanamlandira iye, cifukwa nkhope yace inali yoloza kunka ku Yerusalemu.

54 Ndipo pamene ophunzira ace Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze mota utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?

55 Koma iye anapotoloka nawadzudzula.

56 Ndipo anapita kumudzi kwina.

Matsatidwe a Yesu

57 Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa iye, Ine ndidzakutsatani kumene kuli konse mukapitako.

58 Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe ziri nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.

59 Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga.

60 Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yace ya Ufumu wa Mulungu.

61 Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muthange mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga.

62 Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira cikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24