Luka 11 BL92

Pemphero la Ambuye

1 Ndipo kunali, pakukhala iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ace anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ace.

2 Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze;

3 tipatseni ife tsiku ndi tsiku cakudya ca patsiku.

4 Ndipo mutikhululukire ife macimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.

Fanizo La bwenzi laliuma

5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lace, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;

6 popeza wandidzera bwenzi langa locokera paulendo, ndipo ndiribe compatsa;

7 ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandibvuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa?

8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, cifukwa ali bwenzi lacevkoma cifukwa ca liuma lace adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azisowa.

9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.

10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wace akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?

12 kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa cinkhanira?

13 Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha iye?

Za mwano wa Afarisi

14 Ndipo analikuturutsa ciwanda cosalankhula. Ndipo kunali, citaturuka ciwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15 Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mkuru wa ziwanda amaturutsa ziwanda.

16 Koma ena anamuyesa, nafuna kwa iye cizindikilo cocokera Kumwamba.

17 Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.

18 Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.

19 Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.

20 Koma ngati Ine nditurutsa ziwanda ndi cala ca Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

21 Pamene pali ponse mwini mphamvu alonda pabwalo pace zinthu zace ziri mumtendere;

22 koma pamene pali ponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amcotsera zida zace zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zace.

23 Iye wosabvomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

24 Pamene pali ponse mzimu wonyansa ukaturuka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinaturukako;

25 ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.

26 Pomwepo, upita nutenga mizimu yina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

27 Ndipo kunali, pakunena izi iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.

28 Koma iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.

Cizindikilo ca Yona

29 Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna cizindikilo, ndipo cizindikilo sicidzapatsidwa kwa uwu koma cizindikilo ca Yona.

30 Pakuti monga ngati Yona anali cizindikilo kwa Anineve, cotero adzakhalanso Mwana wa munthu kwa mbadwo uno.

31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza ku'cokera ku malekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomo; ndipo onani, woposa Solomo ali pano.

32 Amuna a ku Nineve adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Y ona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.

Za nyali ya thupi

33 Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'cipinda capansi, kapena pansi pa muyeso, koma pa coikapo cace, kuti iwo akulowamo aone kuunika.

34 Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene pali ponse diso lako liri langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe liri la mdima wokha wokha.

35 Potero yang'anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima.

36 Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lace lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwace ikuunikira iwe.

Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi

37 Ndipo pakulankhula iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.

38 Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba cakudya asanasambe.

39 Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.

40 Opusa inu, kodi iye wopanga kunja kwace sanapanganso m'kati mwace?

41 koma patsani mphatso yacifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse ziri zoyera kwa inu.

42 Koma tsoka inu, Afarisi! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa cakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka ciweruziro ndi cikondi ca Mulungu; mwenzi mutacita izi, ndi kusasiya zinazo.

43 Tsoka inu, Afarisi! cifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kulankhulidwa m'misika.

44 Tsoka inu! cifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa,

45 Ndipo mmodzi wa acilamulo anayankha, nanena kwa iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

46 Ndipo anati, Tsoka inunso, acilamulo inul cifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi cala canu cimodzi.

47 Tsoka inu! cifukwamumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.

48 Comweco muli mboni, ndipo mubvomera nchito za makolo anu; cifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

49 Mwa icinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

50 kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

51 kuyambira mwazi wa 1 Abele kufikira mwazi wa 2 Zakariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kacisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

52 3 Tsoka inu, acilamulo! cifukwa munacotsa cifungulo ca nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.

53 Ndipo pamene iye anaturuka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza iye kolimba, ndi kumtompha iye ndi zinthu zambiri;

54 4 namlindira akakole kanthu koturuka m'kamwa mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24