1 Ndipo kunali lina la masiku awo m'mene iye analikuphunzitsa anthu m'Kacisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe akulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;
2 ndipo anati, nanena naye, Mutiuze mucita in ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene?
3 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze:
4 Ubatizo wa Yohane unacokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?
5 Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena ucokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirira cifukwa ninji?
6 ndiponso, tikanena, Ucokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
7 Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene ucokera.
8 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu izi.
9 Ndipo iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka ku dziko lina, nagonerako nthawi yaikuru.
10 Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wace kwa olima mundawo, kuti ampatseko cipatso ca mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.
11 Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namcitira cipongwe, nambweza, wopanda kanthu.
12 Ndipo anatumizanso wina wacitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja.
13 Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzacita ciani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamcitira iye ulemu.
14 Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzace, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti colowa cace cikhale cathu.
15 Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha, Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawacitira ciani?
16 iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iail
17 Koma iye anawapenyetsa iwo, nati, Nciani ici cinalembedwa,Mwala umene anaukana omanga nyumba,Womwewu unakhala mutu wa pangondya.
18 Munthu yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha.
19 Ndipo alembi ndi ansembe akuru anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.
20 Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ace, kotero kuti akampereke iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.
21 Ndipo anamfunsa iye, nanena, Mphunzitisi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;
22 kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
23 Koma iye anazindikira cinyengo cao, nati kwa iwo,
24 Tandionetsani Ine rupiya latheka. Cithunzithunzi ndi colemba cace nca yani? Anati iwo, Ca Kaisara.
25 Ndipo iye anati kwa iwo, Cifukwa cace perekani kwa Kaisara zace za Kaisara, ndi kwa Mulungu zace za Mulungu.
26 Ndipo sanakhoza kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwace, nakhala cete.
27 Ndipo anadza kwa iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa iye,
28 nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ire, kuti mbale wace wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo ali be mwana iye, mbale wace adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.
29 Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana;
30 ndipo waciwiri,
31 ndi wacitatu anamtenga mkaziyo; ndipo coteronso asanu ndi awiri onse, sanasiya mwana, namwalira.
32 Pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
33 Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.
34 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:
35 koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dzikolijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.
36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.
37 Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Citsamba cija, pamene iye amchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.
38 Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.
39 Ndipo alembi ena anayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino.
40 Pakuti sanalimbanso mtima kumfunsa iye kanthu kena.
41 Koma iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Kristuyo ndiye mwana wa Davine?
42 Pakuti Davine yekha anena m'buku la Masalmo,Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,Ukhale pa dzanja langa lamanja,
43 Kufikira Ine ndikaika adani akopansi pa mapazi ako.
44 Cotero Davine anamchula iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wace bwanji?
45 Ndipo pamene anthu onse anallinkumva iye, anati kwa ophunzira,
46 Cenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda obvala miinjiro, nakonda kulankhulidwa m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamapwando;
47 amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga acita mai pemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.