Luka 21 BL92

Mphatso ya mkazi wamasiye

1 Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni cuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.

2 Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri.

3 Ndipo iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse;

4 pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwace anaikamo za moyo wace, zonse anali nazo.

Yesu aneneratu zam'tsogolo; ciyambi ca masautso

5 Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,

6 Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzace, umene sudzagwetsedwa.

7 Ndipo iwo anamfunsa iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? ndipo cizindikilo ndi cianipamene izi ziti zicitike?

8 Ndipo iye anati, Yang'anirani musasoceretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.

9 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kucitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.

10 Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:

11 ndipo kudzakhala zibvomezi zazikuru, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikilo zazikuru zakumwamba.

12 Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.

13 Kudzakhala kwa inu ngati umboni.

14 Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.

15 Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.

16 Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a pfuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani,

17 Ndipo anthu onse adzadana ndi inu cifukwa ca dzina langa.

18 Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.

19 Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.

Aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu

20 Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira.

21 Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo aturuke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.

22 Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.

23 Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.

24 Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.

Za kubwera kwa Mwana wamunthu

25 Ndipo kudzakhala zizindikilo pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi cisauko ca mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wace wa nyanja ndi mafunde ace;

26 anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekeeera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi;

27 pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru.

28 Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.

29 Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:

30 pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.

31 Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.

32 Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitacitika.

33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.

Khalani odikira

34 Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;

35 pakuti Iidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi.

36 Koma inu dikirani nyengo zonse ndi kupemphera, kutimukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzacitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.

37 Ndipo usana uli wonse iye analikuphunzitsa m'Kacisi; ndi usiku uli wonse anaturuka, nagona pa phiri lochedwa la Azitona.

38 Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa iye kuKacisi kudzamvera Iye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24