Luka 17 BL92

Za zolakwitsa, ndi makhululukidwe, ndi mphamvu ya cikhulupiriro ndi kutumikira kwathu

1 Ndipo anati kwa ophunzira ace, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.

2 Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwace ndi kuponyedwa Iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.

3 Kadzicenjerani nokha; akacimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.

4 Ndipo akakucimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lace, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.

5 Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere cikhulupiriro.

6 Koma Ambuye anati, Mukakhala naco cikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.

7 Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kucokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;

8 wosanena naye makamaka, Undikonzere cakudya me, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?

9 Kodi ayamika kapoloyocifukwa anacita zolamulidwa?

10 Cotero Inunso m'mene mutacita zonse anakulamulirani, Denani, Ife ndife akapolo opanda pace, tangocita zimene tayenera kuzicita.

Yesu aciritsa akhate khumi

11 Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya.

12 Ndipo m'mene analowa iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali;

13 ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, muticitire cifundo.

14 Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa.

15 Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anaciritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akuru;

16 ndipo anagwa nkhope yace pansi ku mapazi ace, namyamika iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.

17 Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwa khumi? koma ali kuti asanu ndi anai aja?

18 Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?

19 Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.

Za kufikanso kwa Ambuye

20 Ndipo pamene Afarisi anamfunsa iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayarikha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;

21 ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.

22 Ndipo anati kwa ophunzira ace, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona.

23 Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! taonani ili! musacoka kapena kuwatsata;

24 pakuti monga mphezi ing'anipa kucokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m'tsiku lace.

25 Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanizidwe ndi mbadwo uno.

26 Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.

27 Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'cingalawa, ndipo cinadza cigumula, niciwaononga onsewo.

28 Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;

29 koma tsiku limene Loti anaturuka m'Sodoma udabvumba mota ndi sulfure zocokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;

30 momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu.

31 Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ace m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zace za m'mbuyo.

32 Kumbukilani mkazi wa Loti,

33 iye ali yense akafuna kusunga moyo wace adzautaya, koma iye ali yense akautaya, adzausunga.

34 Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

35 Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. [

36 ]

37 Ndipo anayankha nanena kwa iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24