Luka 3 BL92

Kulalikira kwa Yohane Mbatizi

1 Ndipo pa caka cakhumi ndi cisanu ca ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode ciwanga ca Galileya, ndi Filipo mbale wace ciwanga ca dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo ciwanga ca Abilene;

2 pa ukuru wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m'cipululu.

3 Ndipo iye anadza ku dziko lonse la m'mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku cikhululukiro ca macimo;

4 monga mwalembedwa m'kalata wa mau a Yesaya mneneri, kuti,Mau a wopfuula m'cipululu,Konzani khwalala la Ambuye,Lungamitsani njira zace.

5 Cigwa ciri conse cidzadzazidwa,Ndipo phiri liri lonse ndi mtunda uti wonse zidzacepsedwa;Ndipo zokhota zidzakhala zolungama,Ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

6 Ndipo anthu onse adzaona cipulumutso ca Mulungu.

7 Cifukwa cace iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anaturukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8 Cifukwa cace balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.

9 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cotero mtengo uli wonse wosabala cipatso cabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

10 Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizicita ciani?

11 Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya acite comweco.

12 Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizicita ciani?

13 Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa cimene anakulamulirani.

14 Ndipo asilikari omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizicita ciani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu ali yense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

15 Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Kristu;

16 Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zace; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

17 amene couluzira cace ciri m'dzanja lace, kuti ayeretse padwale pace, ndi kusonkhanitsa tirigu m'ciruli cace; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.

18 Coteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri.

19 Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula cifukwa ca Herodiya, mkazi wa mbale wace, ndi ca zinthu zonse zoina Herode anazicita,

20 anaonjeza pa zonsezi icinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende.

Yesu abatizidwa

21 Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo,

22 ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Makolo a Yesu

23 Ndipo Yesuyo, pamene anayamba nchito yace, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,

24 mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Melki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,

25 mwana wa Matatio, mwana wa Amosi, mwana wa Naumi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai,

26 mwana wa Maati, mwana wa Matatio, mwana wa Semeini, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda,

27 mwana wa Yoanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri,

28 mwana wa Melki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, rrrvana wa Ere,

29 mwana wa Jose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,

30 mwana wa Simeoni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,

31 mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natanu, mwana wa Davine,

32 mwana wa Jese, mwana wa Obede, mwana wa Boazi, mwana wa Salmoni, mwana wa Naasoni,

33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Ami, mwana wa Ezronu, mwana wa Farese, mwana wa Yuda,

34 mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,

35 mwana wa Seruki, mwana wa Reu, mwana wa Pelege, mwana wa Ebere, mwana wa Sala,

36 mwana wa Kainane, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameke,

37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoke, mwana wa Yaredi, mwana wa Malaleeli, mwana wa Kainane,

38 mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24