1 Ndipo kunali, pakukhala iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ace anati kwa iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ace.
2 Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze;
3 tipatseni ife tsiku ndi tsiku cakudya ca patsiku.
4 Ndipo mutikhululukire ife macimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.
5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lace, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
6 popeza wandidzera bwenzi langa locokera paulendo, ndipo ndiribe compatsa;