28 Koma ngati Mulungu abveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?
29 Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.
30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.
31 Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.
32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.
33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.
34 Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.