30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.
31 Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.
32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.
33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.
34 Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.
35 Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;
36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.