41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?
42 Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace adzamuika kapitao wa pa banja lace, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yace?
43 Wodala kapoloyo amene mbuye wace pakufika, adzampeza alikucita cotero.
44 1 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.
45 Koma 2 kapolo uyo akanena mumtima mwace, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;
46 3 mbuye wa kapolouyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuika dera lace pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
47 Ndipo 4 kapolo uyo, wodziwa cifuniro ca mbuye wace, ndipo sanakonza, ndi kusacita zonga za cifuniro caceco, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.