46 3 mbuye wa kapolouyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuika dera lace pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
47 Ndipo 4 kapolo uyo, wodziwa cifuniro ca mbuye wace, ndipo sanakonza, ndi kusacita zonga za cifuniro caceco, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.
48 Koma 5 iye amene sanacidziwa, ndipo anazicita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu ali yense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
49 Ine ndinadzera kuponya mota pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji, ngati unatha kuyatsidwa?
50 Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!
51 Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapani? Ndinena wa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;
52 pakuti 6 kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.