52 pakuti 6 kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.
53 Adzatsutsana atate ndi mwana wace, ndi mwana ndi atate wace; amace adzatsutsana ndi mwana wamkazi'l ndi mwana wamkazi ndi amace, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wace, ndi mkaziyo ndi mpongozi wace.
54 Koma iye ananenanso kwa makamu a anthu, 7 Pamene pali ponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.
55 Ndipo pamene mphepo ya kumwela iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.
56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengoyino?
57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?
58 Pakuti 8 pamene ulikupita naye mnzako wa miandu kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikari, ndi msilikari angaponye iwe m'nyumba yandende.