7 Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna cipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pace?
8 Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale caka cino comwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;
9 ndipo, ngati udzabala cipatso kuyambira pamenepo, cabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.
10 Ndipo analikuphunzitsa m'sungagoge mwina, tsiku la Sabata.
11 Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.
12 Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.
13 Ndipo anaika manja ace pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.