17 Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwa khumi? koma ali kuti asanu ndi anai aja?
18 Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu?
19 Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe.
20 Ndipo pamene Afarisi anamfunsa iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayarikha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;
21 ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu.
22 Ndipo anati kwa ophunzira ace, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu, koma simudzaliona.
23 Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! taonani ili! musacoka kapena kuwatsata;