10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;
11 pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.
12 Ndipo ici ndi cizindikilo kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsaru atagonamodyera.
13 Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,
14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.
15 Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.
16 Ndipo iwo anadza ndi cangu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.