13 Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,
14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,Ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.
15 Ndipo panali, pamene angelo anacokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzace, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone cinthu ici cidacitika, cimene Ambuye anatidziwitsira ife.
16 Ndipo iwo anadza ndi cangu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.
17 Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.
18 Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.
19 Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.