29 Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja,Lolani ine, kapolo wanu, ndicoke mumtendere;
30 Cifukwa maso anga adaona cipulumutso canu,
31 Cimene munakonza pamaso pa anthu onse,
32 Kuunika kukhale cibvumbulutso ca kwa anthu a mitundu,Ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.
33 Ndipo atate ndi amace anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za iye.
34 Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Mariya amace, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa. Israyeli; ndipo akhale cizindikilo cakutsutsana naco;
35 eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.