37 zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zace: makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sanacoka kuKacisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
38 Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za iye kwa anthu onse 1 akuyembekeza ciombolo ca Yerusalemu.
39 Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa cilamulo ca Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mudzi kwao, ku Nazarete.
40 Ndipo 2 mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi cisomo ca Mulungu cinali pa iye.
41 Ndipo atate wace ndi amace 3 akamuka caka ndi caka ku Yerusalemu ku Paskha.
42 Ndipo pamene iye anakhala ndi zaka zace khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga macitidwe a phwando;
43 ndipo pakumariza masiku ace, pakubwera iw, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amace sanadziwa;