4 Ndipo Yosefe yemwe anakwera kucokera ku Galileya, ku mudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, ku mudzi wa Davine, dzina lace Betelehemu, cifukwa iye anali wa banja ndi pfuko lace la Davine;
5 kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati,
6 Ndipo panali pokhaia iwo komweko, masiku ace a kubala anakwanira.
7 Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.
8 Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.
9 Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.
10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;