6 Ndipo panali pokhaia iwo komweko, masiku ace a kubala anakwanira.
7 Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.
8 Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.
9 Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.
10 Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;
11 pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.
12 Ndipo ici ndi cizindikilo kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsaru atagonamodyera.