32 Pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
33 Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.
34 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:
35 koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dzikolijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.
36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa.
37 Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Citsamba cija, pamene iye amchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.
38 Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.