16 Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a pfuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani,
17 Ndipo anthu onse adzadana ndi inu cifukwa ca dzina langa.
18 Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.
19 Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.
20 Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira.
21 Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo aturuke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.
22 Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.