18 Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.
19 Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.
20 Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira.
21 Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo aturuke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.
22 Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.
23 Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.
24 Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.