58 Ndipo 9 popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine.
59 Ndipo 10 patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya.
60 Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa cimene ucinena, Ndipo pomwepo, iye ali cilankhulire, tambala analira.
61 Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo 11 Petra anakumbukila mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, 12 Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.
62 Ndipo anaturuka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.
63 Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza iye, nampanda.
64 Ndipo anamkulunga iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani?