1 Koma tsiku loyamba la sabata, mbanda kuca, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza.
2 Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuucotsa pamanda.
3 Ndipo m'mene analowa sanapeza mtembo wa Ambuye Yesu.
4 Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;
5 ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?