30 Ndipo kunali m'mene iye anaseama nao pacakudya, anatenga mkate, naudalitsa naunyema, napatsa iwo.
31 Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira iye; ndipo anawakanganukira iye, nawacokera.
32 Ndipo anati wina kwa mnzace, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitseguliramalembo?
33 Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,
34 nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.
35 Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate.
36 Ndipo pakulankhula izi iwowa, iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.