4 Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;
5 ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
6 Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,
7 ndi kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.
8 Ndipo anakumbukila mau ace, nabwera kucokera kumanda,
9 nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.
10 Koma panali Mariya wa Magadala, ndi Y ohana, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.