6 Ndipo anthu onse adzaona cipulumutso ca Mulungu.
7 Cifukwa cace iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anaturukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
8 Cifukwa cace balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.
9 Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cotero mtengo uli wonse wosabala cipatso cabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.
10 Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizicita ciani?
11 Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya acite comweco.
12 Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizicita ciani?