1 Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;
2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adaturuka m'menemo, nalikutsuka makoka ao.
3 Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.
4 Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.