3 Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.
4 Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.
5 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.
6 Ndipo pamene anacita ici, anazinga unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika;
7 ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.
8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa.
9 Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;