1 BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2 Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ace;
3 ndi Yuda anabala Farese ndi Zara mwa Tamare; ndi Farese anabala Ezronu; ndi Ezronu anabala Aramu;
4 ndi Aramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni;
5 ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese;
6 ndi Jese anabala Davide mfumuyo.Ndipo Davide anabala Solomo mwa mkazi wa Uriya;