1 Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ace khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuiturutsa, ndi yakuciza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.
2 Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wochedwa Petro, ndi Andreya mbale wace; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace;
3 Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
4 Simoni Mkanani, ndi Yudasi Isikariote amenenso anampereka Iye.
5 Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti,Musapite ku njira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
6 koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli.