25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wace, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamucha mwini banja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ace?
26 Cifukwa cace musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika.
27 Cimene ndikuuzani inu mumdima, tacinenani poyera; ndi cimene mucimva m'khutu, mucilalikire pa macindwi nyumba.
28 Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'gehena.
29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:
30 komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.
31 Cifukwa cace musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.