19 Sadzalimbana, sadzapfuula;Ngakhale mmodzi sadzamva mau ace m'makwalala;
20 Bango lophwanyika sadzalityola,Ndi nyali yofuka sadzaizima,Kufikira Iye adzatumiza ciweruzo cikagonjetse,
21 Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lace.
22 Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi ciwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamciritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.
23 Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?
24 Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samaturutsa ziwanda koma ndi mphamvu yace ya Beelzebule, mkuru wa ziwanda.
25 Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uti wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uti wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;