44 Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino:
46 ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi 1 kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse;
48 limene podzala, analibvuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.
49 Padzatero pa cimariziro ca nthawi ya pansi pano: angelo adzaturuka, 2 nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,
50 nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.