5 Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera;
6 ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.
7 Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo.
8 Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.
9 Amene ali ndi makutu, amve.
10 Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
11 Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.