28 Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, cikhulupiriro cako ndi cacikuru; cikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wace anacira nthawi yomweyo.
29 Ndipo Yesu anacoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo.
30 Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ace: ndipo Iye anawaciritsa;
31 kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nacira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.
32 Ndipo Yesu anaitana ophunzira ace, nati, Mtima wanga ucitira cifundo khamu la anthuwa, pakuti ali cikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira,
33 Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'cipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu?
34 Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono.