1 Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse cizindikiro ca Kumwamba.
2 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwe; popeza thambo liri laceza.
3 Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo; popeza thambo liri la ceza codera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yin o, simungathe kuzindikira.
4 Obadwa oipa ndi acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sadzalandira cizindikiro cina, koma cizindikiro ca Yona. Ndipo Iye anawasiya, nacokapo.
5 Ndipo ophunzira anadza ku tsidya linalo, naiwala kutenga mikate.
6 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi ndi Asaduki.