14 Comweco siciri cifuniro ca Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.
15 Ndipo ngati mbale wako akucimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.
16 Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.
17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
18 Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.
19 Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri ainu abvomerezana pansi pano cinthu ciri conse akacipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawacitira.
20 Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndiri komweko pakati pao.