21 Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? kufikira kasanu ndi kawiri kodi?
22 Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi ananu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.
23 Cifukwa cace Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ace.
24 Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.
25 Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wace analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wace ndi ana ace omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.
26 Cifukwa cace kapoloyo anagwadapansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.
27 Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi cisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.