7 Iwo ananena kwa Iye, Nanga cifukwa ninji Mose analamulira kupatsa kalata wa cilekaniro, ndi kumcotsa?
8 Iye ananena kwa iwo, Cifukwa ca kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kucotsa akazi anu; koma paciyambi sikunakhala comweco.
9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akacotsa mkazi wace, kosakhala cifukwa ca cigololo, nadzakwatira wina, acita cigololo: ndipo iye amene akwatira wocotsedwayo, acita cigololo.
10 Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wace uti wotere, sikuli kwabwino kukwatira.
11 Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira conena ici, koma kwa iwo omwe capatsidwa.
12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, cifukwa ca Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ici acilandire.
13 Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ace pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula.