16 Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'miraga yace yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
17 Pomwepo cinacitidwa conenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,
18 Mau anamveka m'Rama,Maliro ndi kucema kwambiri;Rakele wolira ana ace,Wosafuna kusangalatsidwa,Cifukwa palibe iwo.
19 Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe m'Aigupto,
20 nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amace, nupite ku dziko la Israyeli: cifukwa anafa uja wofuna moyo wace wa kamwanako.
21 Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amace, nalowa m'dziko la Israyeli.
22 Koma pakumva iye kuti Arikelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wace Herode, anacita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anacenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa ku dziko la Galileya,