25 Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akuru ao amacita ufumu pa iwo.
26 Sikudzakhala comweco kwa inu ai; koma amene ali yense akafuna kukhala warnkuru mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
27 ndipo amene ali yense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:
28 monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.
29 Ndipo pamene iwo analikuturuka m'Yeriko, khamu lalikuru la anthu linamtsata Iye.
30 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'rnphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anapfuula nati, Muticitire ife cifundo, Inu Mwana wa Davide.
31 Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, muticitire cifundo, Inu Mwana wa Davide.