19 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okha okha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso cipatso ku nthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.
20 Ndipo ophunzira poona ici anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?
21 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala naco cikhulupiriro, osakayika-kayika, mudzacita si ici ca pa mkuyu cokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nvania, cidzacitidwa.
22 Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.
23 Ndipo m'mene Iye analowa m'Kacisi, ansembe akuru ndi akuru anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Mucita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi:
25 Ubatizo wa Yohane, ucokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzace, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?