10 Ndipo akapolo ao anaturukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pacakudya.
11 Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;
12 nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala naco cobvala ca ukwati? Ndipo iye analibe mau.
13 Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye ku mdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
14 Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.
15 Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwace.
16 Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu ali yense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.