26 cimodzimodzi waciwiri, ndi wacitatu, kufikira wacisanu ndi ciwiri.
27 Ndipo pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
28 Cifukwa cace m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? pakuti onse anakhala naye.
29 Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa a osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.
30 Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.
31 Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi comwe cinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
32 Ine ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.