39 Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
40 Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.
41 Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa,
42 nati, Muganiza bwanji za Kristu? ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.
43 Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amchula Iye bwanji Ambuye, nanena,
44 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,Ukhale pa dzanja lamanja langa,Kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.
45 Cifukwa cace ngati Davide amchula Iye Ambuye, ali mwana wace bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.