42 nati, Muganiza bwanji za Kristu? ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.
43 Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amchula Iye bwanji Ambuye, nanena,
44 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,Ukhale pa dzanja lamanja langa,Kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.
45 Cifukwa cace ngati Davide amchula Iye Ambuye, ali mwana wace bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.
46 Ndipo sanalimbika mtima munthu ali yense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.