5 Koma iwo ananyalanyaza, nacoka, wina ku munda wace, wina ku malonda ace:
6 ndipo otsala anagwira akapolo ace, nawacitira cipongwe, nawapha.
7 Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.
8 Pomwepo inanena kwa akapolo ace, Za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera.
9 Cifukwa cace pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene ali yense mukampeze, itanani kuukwatiku.
10 Ndipo akapolo ao anaturukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pacakudya.
11 Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;