36 wamarisece Ine, ndipo munandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kuceza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.
37 Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? kapena waludzu, ndi kukumwetsani?
38 Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucerezani? kapena wamarisece, ndi kukubvekani?
39 Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?
40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munacitira ici mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandicitira ici Ine.
41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku mota wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace:
42 pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine: